1. Ambuye inu, citirani akapolo anu colungama ndi colingana; podziwa kuti inunso muli naye Mbuye m'Mwamba.
2. Citani khama m'kupemphera, nimudikire momwemo ndi ciyamiko;
3. ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule cinsinsi ca Kristu; cimenenso ndikhalira m'ndende,