4. Pamene Kristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi iye m'ulemerero.
5. Cifukwa cace fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, cidetso, cifunitso ca manyazi, cilakolako coipa, nelicisiriro, cimene ciri kupembedza mafano;
6. cifukwa ca izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;
7. zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo,
8. Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu:
9. musamanamizana wina ndi mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,
10. ndipo munabvala watsopano, amene alikukonzekawatsopano, kuti akhale naco cizindikiritso, mousa mwa cifaniziro ca iye amene anamlenga iye;
11. pamene palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wachedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Kristu ndiye zonse, ndi m'zonse.