12. Pakuti mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi cifukwa ca nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za ciyambidwe ca maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati cakudya cotafuna.
13. Pakuti yense wakudya mkaka alibe cizolowezi ca mau a cilungamo; pakuti ali khanda.
14. Koma cakudya cotafuna ciri ca anthu akulu misinkhu, amene mwa kucita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zao kusiyanitsa cabwino ndi coipa.