Ahebri 3:17-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Koma anakwiya ndi ayani zaka makumi anai? Kodi si ndi awo adacimwawo, amene matupi ao adagwa m'cipululu?

18. Ndipo adawalumbirira ayani kuti asalowe mpumulo wace?

19. Si awo kodiosamverawo? Ndipo tiona kuti sanakhoza kulowa cifukwa ca kusakhulupirira.

Ahebri 3