11. Monga ndinalumbira m'ukali wanga:Ngati adzalowa mpumulo wanga!
12. Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;
13. komatu dandauliranani nokha tsiku ndi tsiku, pamene paehedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi cenjerero la ucimo;
14. pakuti takhala ife olandirana ndi Kristu, ngatitu tigwiritsa ciyambi ca kutama kwathu kucigwira kufikira citsiriziro;
15. umo anenamo,Lero ngati mudzamva mau ace,Musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima.
16. Pakuti ndi ayani, pakumva, anapsetsa mtima? Kodi si onse aja adaturuka m'Aigupto ndi Mose?