11. Chango ciri conse, pakucitika, sicimveka cokondwetsa, komatu cowawa; koma citatha, cipereka cipatso ca mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa naco, ndico ca cilungamo.
12. Mwa ici limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka;
13. ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti cotsimphinaco cisapatulidwe m'njira, koma ciciritsidwe.
14. Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi ciyeretso cimene, akapanda ici, palibe mmodzi adzaona Ambuye:
15. ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera cisomo ca Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungabvute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;
16. kuti pangakhale wacigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wace wobadwa nao mtanda umodzi wa cakudya.