Ahebri 12:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cifukwa cace ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukuru wotere wa mboni, titaye colemetsa ciri conse, ndi cimoli Iimangotizinga, ndipo tithamange mwacipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womariza wa cikhulupiriro cathu,

2. Yesu, ameneyo, cifukwa ca cimwemwe coikidwaco pamaso pace, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wacifumu wa Mulungu,

Ahebri 12