Ahebri 11:24-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndi cikhulupiriro Mose, atakula msinkhu, anakana kuchedwa mwana wace wa mwana wamkazi wa Farao;

25. nasankhula kucitidwa zoipa pamodzi ndi anthu a Mulungu, kosati kukhala nazo zokondweretsa za zoipa nthawi;

26. nawerenga thonzo la Kristu cuma coposa zolemera za Aigupto; pakuti anapenyerera cobwezera ca mphotho.

27. Ndi cikhulupiriro anasiya Aigupto, wosaopa mkwiyo wa mfumu; pakuti anapirira molimbika monga ngari kuona wosaonekayo.

28. Ndi cikhulupiriro 1 anacita Paskha, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo.

29. Ndi cikhulupiriro 2 anaoloka Nyanja Yofiira kupita ngati pamtunda: ndiko Aaigupto poyesanso anamizidwa.

30. Ndi cikhulupiriro 3 malinga a Yeriko adagwa atazunguliridwa masiku asanu ndi awiri.

31. Ndi cikhulupiriro 4 Rahabi wadama uja sanaonongeka pamodzi ndi osamverawo, popeza analandira ozonda ndi mtendere.

32. Ndipo ndinene cianinso? pakuti idzandiperewera nthawi ndifotokozere za 5 Gideoni, 6 Baraki, 7 Samsoni, 8 Yefita; za 9 Davide, ndi 10 Samueli ndi aneneri;

Ahebri 11