15. Ndipotu akadakumbukila lijalo adaturukamo akadaona njira yakubwera nayo.
16. Koma tsopano akhumba lina loposa, ndilo la m'Mwamba; mwa ici Mulungu sacita manyazi nao poitanidwa Mulungu wao; pakuti adawakonzera mudzi.
17. Ndi cikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isake, ndipo iye amene adalandira malonjezano anapereka mwana wace wayekha;
18. amene kudanenedwa za iye, kuti, Mwa Isake mbeu yako idzaitanidwa:
19. poyesera iye kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa, ngakhale kwa akufa; kucokera komwe, paciphiphiritso, anamlandiranso.
20. Ndi cikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau, zingakhale za zinthu zirinkudza,