9. pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzacita cifuniro canu. Acotsa coyambaco, kuti akaike caciwirico.
10. Ndi cifuniro cimeneco tayeretsedwa mwa copereka ca thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.
11. Ndipotu wansembe ali yenseamaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawiri kawiri, zimene sizikhoza konse kucotsa macimo;
12. koma iye, m'mene adapereka nsembe imodzi cifukwa ca macimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu cikhalire;