Agalatiya 6:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa cifatso; ndikudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.

2. Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse cilamulo ca Kristu.

3. Pakuti ngati wina ayesa ali kanthu pokhala ali cabe, adzinyenga yekha.

Agalatiya 6