11. Koma ine, abale, ngati ndilalikiransoindulidwe, ndizunzikanso bwanji? Pamenepo cikhumudwitso ca mtanda cidatha.
12. Mwenzi atadzidula, iwo akugwedezetsani inu.
13. Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; cokhaco musacite nao ufulu wanu cothandizira thupi, komatu mwa cikondi citiranani ukapolo.
14. Pakuti mau amodzi akwaniritsa cilamulo conse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.
15. Koma ngati mulumana ndi kudyana, cenjerani mungaonongane.
16. Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse cilakolako ca thupi.