Agalatiya 4:21-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndiuzeni, inu akufuna kukhala omvera lamulo, kodi simukumva cilamulo?

22. Pakuti palembedwa, kuti Abrahamu anali nao ana amuna awiri, mmodzi wobadwa mwa mdzakazi, ndi mmodzi wobadwa mwa mfulu.

23. Komatu uyo wa mdzakazi anabadwa monga mwa thupi; koma iye wa mfuluyo, anabadwa monga mwa Ionjezano, Izo ndizo zophiphiritsa;

Agalatiya 4