13. Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Bamabanso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao.
14. Komatu pamene ndinaona kuti sanalikuyenda koongoka, monga mwa coonadi ca Uthenga Wabwino, ndinati kwa Kefa pamaso pa onse, Ngati inu muli Myuda mutsata makhalidwe a amitundu, ndipo si a Ayuda, mukangamiza bwanji amitundu atsate makhalidwe a Ayuda?
15. Ife ndife Ayuda pacibadwidwe, ndipo sitiri ocimwa a kwaamitundu;