Agalatiya 2:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo popita zaka khumi ndi zinai ndinakweranso kunka ku Yerusalemu pamodzi ndi Bamaba, ndinamtenganso Tito andiperekeze.

2. Koma ndinakwera kunkako mobvumbulutsa; ndipo ndinawauza Uthenga Wabwino umene ndiulalikira kwa amitundu; koma m'tseri kwa iwo omveka, kuti kapena ndingathamange, kapena ndikadathamanga cabe.

Agalatiya 2