12. Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikacigwire ici cimene anandigwirira Yesu Kristu.
13. Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kucigwira: koma cinthu cimodzi ndicicita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,
14. ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu.
15. Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ici mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzabvumbulutsira inu;
16. cokhaci, kumene tidafikirako, mayendedwe athu alinganeko.