19. amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti acite cidetso conse mu umbombo.
20. Koma inusimunaphunzira Kristu cotero,
21. ngatitu mudamva iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa iye, monga coonadi ciri mwa Yesu;
22. kuti mubvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wobvunda potsata zilakolako za cinyengo;
23. koma kuti 1 mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu,