12. amene tiri naye cokhazikika mtima ndi ciyandiko eolimbika, mwa cikhulupiriro ca pa iye.
13. Mwa ici ndipempha kuti musade mtima, m'zisautso zanga cifukwa ca inu, ndiwo ulemerero wanu.
14. Cifukwa ca ici ndipinda maondo anga kwa Atate,
15. amene kucokera kwa iye pfuko lonse la m'mwamba ndi la padziko alicha dzina,
16. kuti monga mwa cuma ca ulemerero wace akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wace, m'kati mwanu,