3. amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kucita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo cibadwire, monganso otsalawo;
4. koma Mulungu, wolemera cifundo, cifukwa ca cikondi cace cacikuru cimene anatikonda naco,
5. tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Kristu (muli opulumutsidwa ndi cisomo),
6. ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Kristu Yesu;
7. kuti akaonetsere m'nyengo zirinkudza cuma coposa ca cisomo cace, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Kristu Yesu.
8. Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu;
9. cosacokera kunchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense.
10. Pakuti ife ndife cipango cace, olengedwa mwa Kristu Yesu, kucita nchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.
11. Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, ochedwa kusadulidwa ndi iwo ochedwa mdulidwe m'thupi, umene udacitika ndi manja;
12. kuti nthawi ija munali opanda Kristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israyeli, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda ciyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.