Aefeso 2:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zocimwa zanu,

2. zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakucita tsopano mwa ana a kusamvera;

3. amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kucita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo cibadwire, monganso otsalawo;

Aefeso 2