6. amene anacita umboni za cikondi cako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzacita bwino:
7. pakuti cifukwa ca dzinali anaturuka, osalandira kanthu kwa amitundu.
8. Cifukwa cace ife tiyenera kulandira otere, kuti tikakhale othandizana naco coonadi,
9. Ndalemba kanthu kwa Mpingo; komatu Diotrefe uja, wofuna kukhala wamkuru wa iwo, satilandira ife.
10. Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa nchito zace zimene aeitazi, zakunena zopanda pace pa ife ndi mau oipa; ndipopopeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powaturutsa mu Mpingo,