4. Ndiribe cimwemwe coposa ici, cakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m'coonadi.
5. Wokondedwa, ucita cokhulupirika naco ciri conse, uwacitira abale ndi alendo omwe;
6. amene anacita umboni za cikondi cako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzacita bwino:
7. pakuti cifukwa ca dzinali anaturuka, osalandira kanthu kwa amitundu.