12. Demetriyo, adamcitira umboni anthu onse, ndi coonadi comwe; ndipo ifenso ticita umboni; ndipo udziwa kuti umboni wathu uli woona.
13. Ndinali nazo zambiriza kukulembera, komatu sindifuna kukulembera ndi kapezi ndi peni;
14. koma ndiyembekeza kukuona iwe msanga, ndipo tidzalankhula popenyana, Mtendere ukhale nawe. Akulankhula abwenzi, Lankhula abwenzi ndi kuchula maina ao.