3 Yohane 1:11-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Wokondedwa, usatsanza ciri coipa komatu cimene ciri cokoma. Iye wakucita cokoma acokera kwa Mulungu; ye wakucita coipa sanamuona Mulungu.

12. Demetriyo, adamcitira umboni anthu onse, ndi coonadi comwe; ndipo ifenso ticita umboni; ndipo udziwa kuti umboni wathu uli woona.

13. Ndinali nazo zambiriza kukulembera, komatu sindifuna kukulembera ndi kapezi ndi peni;

14. koma ndiyembekeza kukuona iwe msanga, ndipo tidzalankhula popenyana, Mtendere ukhale nawe. Akulankhula abwenzi, Lankhula abwenzi ndi kuchula maina ao.

3 Yohane 1