2 Yohane 1:10-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Munthu akadza kwa inu, wosatenga ciphunzitso ici, musamlandire iye kunyumba, ndipo musamlankhule.

11. Pakuti iye wakumlankhula ayanjana nazo nchito zace zoipa.

12. Pokhala ndiri nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kucita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti cimwemwecanucikwanire.

13. Akulankhulani ana a mbale wanu wosankhika.

2 Yohane 1