2 Timoteo 3:9-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwao kudzaonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja.

10. Koma iwe watsatatsata ciphunzitso canga, mayendedwe, citsimikizo mtima, cikhulupiriro, kuleza mtima, cikondi, cipiriro,

11. mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandicitira m'Antiokeya, m'Ikoniya, m'Lustro, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.

2 Timoteo 3