10. koma caonetsedwa tsopano m'maonekedwe a Mpulumutsi wathu Kristu Yesu, amenedi anatha imfa, naonetsera poyera moyo ndi cosabvunda mwa Uthenga Wabwino,
11. umene ndaikikapo mlaliki, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wace.
12. Cifukwa ca ideo ndinamva zowawa izi; komatu sindicita manyazi; pakuti ndimdziwa iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira cosungitsa eangaeo kufikira tsiku lijalo.