23. Ndipo mfumu inanena ndi Simeyi, Sudzafa. Mfumu nimlumbirira iye.
24. Ndipo Mefiboseti mwana wa Sauli anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasamba mapazi ace, kapena kumeta ndebvu zace, kapena kutsuka zobvalazace kuyambira tsiku lomuka mfumukufikira tsiku lobwera kwao mumtendere.
25. Ndipo kunali pakufika iye ku Yerusalemu kukakomana ndi mfumu, mfumu inanena naye, Cifukwa ninji sunapita nane Mefiboseti?
26. Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira buru kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndiri wopunduka.