35. Ndipo suli nao kumeneko Zadoki ndi Abyatara ansembewo kodi? motero ciri conse udzacimva ca m'nyumba ya mfumu uziuza Zadoki ndi Abyatara ansembewo.
36. Onani, ali nao komweko ana amuna ao awiri, Ahimaazi mwana wa Zadoki, ndi Jonatani mwana wa Abyatara; iwowa muwatumize kuti adzandiuze ciri conse mudzacimva.
37. Comweco Husai bwenzi la Davide anadza m'mudzimo; ndipo Abisalomu anafika ku Yerusalemu.