2 Samueli 12:3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ace. Kanadyako cakudya cace ca iye yekha, kanamwera m'cikho ca iye yekha, kanagona pa cifukato cace, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wace wamkazi.

2 Samueli 12

2 Samueli 12:1-4