2 Samueli 11:3-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu mkazi wa Uriya Mhiti?

4. Ndipo bavide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adacoka mumsambo; ndipo anabwereranso ku nyumba yace.

5. Ndipo mkaziyo anaima, natumiza munthu nauza Davide, kuti, Ndiri ndi pakati.

6. Davide natumiza kwa Yoabu, nati, Unditumizire Uriya Mhiti. Ndipo Yoabu anatumiza Uriya kwa Davide.

7. Ndipo pakufika kwa iye Uriya uja, Davide anamfunsa kuti, Yoabu ali bwanji? ndi anthu ali bwanji? ndi nkhondo iri bwanji?

2 Samueli 11