2 Samueli 10:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali zitapita izi, mfumu ya ana a Amoni inamwalira, ndipo Hanuni mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

2. Ndipo Davide anati, Ndidzacitira Hanuni mwana wa Nahasi zokoma, monga atate wace anandicitira ine zokoma. Comweco Davide anatumiza ndi dzanja la anyamata ace kuti akamsangalatse cifukwa ca atate wace. Ndipo anyamata a Davide anafika ku dziko la ana a Amoni.

2 Samueli 10