1. Okondedwa, uyu ndiye kalata waciwiri ndilembera kwa inu tsopano; mwa onse awiri nditsitsimutsa mtima wanu woona ndi kukukumbutsani;
2. kuti mukumbukile mau onenedwa kale ndi aneneri oyera, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi, mwa atumwi anu;
3. ndi kuyamba kucizindikira ici kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kucita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,
4. ndi kunena, Liri kuti lonjezano la kudza kwace? pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga ciyambire cilengedwe.