2 Petro 1:17-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera iye mao otere ocokera ku ulemerero waukuru, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye;

18. ndipo mau awa ocokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi iye m'phiri lopatulika lija,

19. Ndipo tiri nao mau a cinenero okhazikika koposa; amene mucita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukaca, nikauka nthanda pa mtima yanu;

20. ndi kudziwa ici poyamba, kuti palibe cinenero ca lembo citanthauzidwa pa cokha,

21. pakuti kale lonse cinenero sicinadza ndi cifuniro ca munthu; koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.

2 Petro 1