2. Koma ndakumangirani nyumba yokhalamo, malo okhazikika okhalamo Inu nthawi yosatha.
3. Ndipo mfumu inapotolokera nkhope yace, nidalitsa khamu lonse la Israyeli; ndi khamu lonse la Israyeli linaimirira.
4. Nati iye, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, wakunena m'kamwa mwace ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa: ndi manja ace, ndi kuti,
5. Kuyambira tsiku lakuturutsa Ine anthu anga m'dziko la Aigupto, sindinasankha mudzi uli wonse m'mafuko onse a Israyeli, kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, kapena kusankha munthu ali yense akhale kalonga wa anthu anga Israyeli;
6. koma ndinasankha Yerusalemu, kuti dzina langa likhale komweko; ndinasankhanso Davide akhale mfumu ya anthu anga Israyeli.