1. Momwemo zidatha nchito zonse Solomo adazicitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomo anabwera nazo zopatulika zija za atate wace Davide; naziika siliva, ndi golidi, ndi zipangizo zonse m'cuma ca nyumba ya Mulungu.Kuperekedwa kwa Kacisi.
2. Pamenepo Solomo anasonkhanitsira akulu akulu a Israyeli, ndi akuru onse a mafuko, ndi akalonga a nyumba za makolo a ana a Israyeli, ku Yerusalemu, kukatenga likasa la cipangano ca Yehova ku mudzi wa Davide ndiwo Zioni.
3. Ndipo amuna onse a Israyeli anasonkhana kwa mfumu kumadyerero anacitikawo, m'mwezi wacisanu ndi ciwiri.
4. Nadza akulu akulu onse a Israyeli, nanyamula likasalo Alevi.
5. Ndipo anakwera nalo likasa, ndi cihema cokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika zinali m'cihemamo; izizo ansembe Alevi anakwera nazo.
6. Ndi mfumu Solomo ndi khamu lonse la Israyeli losonkhana kwa iye anali kulikasa, naphera nsembe, nkhosa ndi ng'ombe zosawerengeka kucuruka kwace.