1. Ndipo a Solomo anati alimangire dzina la Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wace.
2. Nawerenga Solomo amuna zikwi khumi mphambu makumi asanu ndi limodzi osenza mirimo, ndi amuna zikwi makumi asanu ndi atatu otema mitengo m'mapiri, ndi zikwi zitatu mphambu mazana asanu ndi limodzi kuwayang'anira.