12. Ndipo Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Yuda, nathawa Akusi.
13. Ndi Asa ndi anthu anali naye anawalondola mpaka ku Gerari, nagwa Akusi ambiri osalimbikanso mphamvu iwowa; pakuti anathyoledwa pamaso pa Yehova ndi ankhondo ace; ndipo anatenga zofunkha zambiri.
14. Ndipo anakantha midzi yonse pozungulira pace pa Gerari; a pakuti mantha ocokera kwa Yehova anawagwera; ndipo anafunkha m'midzi monse, pakuti mudacuruka zofunkha m'menemo.
15. Anakanthanso a m'mahema a ng'ombe, nalanda nkhosa zocuruka, ndi ngamila; nabwerera kumka ku Yerusalemu.