1. Momwemo Abiya anagona ndi makolo ace, ndipo anamuika m'mudzi wa Davide; ndi Asa mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace, m'masiku ace dziko linaona bata zaka khumi.
2. Ndipo Asa anacita cokoma ndi coyenera m'maso mwa Yehova Mulungu wace,
3. nacotsa maguwa a nsembe acilendo, ndi misanje; naphwanya zoimiritsa zao, nalikha zifanizo zao,
4. nauza Yuda afune Yehova Mulungu wa makolo ao, ndi kucita cilamulo ndi cowauza, Iye.
5. Anacotsanso m'midzi yonse ya Yuda misanje, ndi zifanizo za dzuwa; ndi ufumuwo unacita bata pamaso pace.