18. Pamenepo Rehabiamu mfumu inatuma Hadoramu woyang'anira thangata; koma ana a Israyeli anamponya miyala, nafa. Ndipo Rehabiamu mfumu anafulumira kukwera pa gareta wace kuthawira ku Yerusalemu.
19. Motero Israyeli anapandukana nayo nyumba ya Yuda mpaka lero lino.