11. Ndipo linadza tsiku lakuti anafikako, nalowa m'cipinda cosanja, nagona komweko.
12. Nati kwa Gehazi mnyamata wace, Itana Msunemu uja. Namuitana, naima mkaziyo pamaso pace.
13. Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikucitire iwe ciani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga.
14. Pamenepo anati, Nanga timcitire iye ciani? Nati Gehazi, Zedi alibe mwana, ndi mwamuna wace wakalamba.
15. Nati, Kamuitane. Namuitana, naima pakhomo mkaziyo.