2 Mafumu 4:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anapfuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ace.

2. Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikucitire ciani? undiuze m'nyumba mwako muli ciani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta.

3. Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang'ono.

2 Mafumu 4