2 Mafumu 3:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israyeli m'Samariya m'caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.

2. Nacita coipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wace ndi amace; pakuti anacotsa coimiritsa ca Baala adacipanga atate wace.

3. Koma anakangamira zoipa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene anacimwitsa nazo Israyeli, osalekana nazo.

2 Mafumu 3