2 Mafumu 25:28-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. nakamba naye zokoma, namkweza mpando wace waulemu upose mipando ya mafumu anali pamodzi naye m'Babulo.

29. Nasintha zobvala zace za m'kaidi, namadya iye mkate pamaso pace masiku onse a moyo wace.

30. Ndi kunena za cakudya cace, panali cakudya cosalekeza copatsidwa kwa iye ndi mfumu, tsiku Uri lonse gawo lace, masiku onse a moyo wace.

2 Mafumu 25