2 Mafumu 23:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo laciwiri, ndi olindira pakhomo, aturutse m'Kacisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi cifanizo cija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lace kumka nalo ku Beteli.

5. Naletsa ansembe opembedza mafano, amene mafumu a Yuda anawaika afukize zonunkhira pa misanje m'midzi ya Yuda, ndi pamalo pozinga Yerusalemu; wo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.

6. Naturutsa cifanizoco m'nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nacitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nacipera cikhale pfumbi, naliwaza pfumbi lace pa manda a ana a anthu.

7. Nagamula nyumba za anyamata adama okhala ku nyumba ya Yehova, kumene akazi anaomba nsaru zolenjeka za cifanizoco.

2 Mafumu 23