6. Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti mubwebvuke kwa mbale yense wakuyenda dwacedwace, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.
7. Pakuti mudziwa nokha m'mene muyenera kutitsanza ifemo; pakuti sitinakhala dwacedwace mwa inu;
8. kapena sitinadya mkate cabe pa dzanja la munthu ali yense, komatu m'cibvuto ndi cipsinjo, tinagwira nchito usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu;
9. si cifukwa tiribe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu citsanzo canu, kuti mukatitsanze ife.
10. Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ici, Ngati munthu safuna kugwira nchito, asadyenso.