7. Pakuti cinsinsi ca kusayeruzika cayambadi kucita; cokhaci pali womletsa tsopano, kufikira akamcotsa pakati.
8. Ndipo pamenepo adzabvumbulutsidwa wosayeruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pace, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwace;
9. ndiye amene kudza kwace kuli monga mwa macitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikilo ndi zozizwa zonama;
10. ndi m'cinyengo conse ca cosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza cikondi ca coonadi sanacisandira, kuti akapulumutsidwe iwo.
11. Ndipo cifukwa cace Mulungu atumiza kwa iwo macitidwe a kusoceretsa, kuti akhulupirire bodza;
12. kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirira coonadi, komatu anakondwera ndi cosalungama.
13. Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa: ca inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira paciyambi, mulandire cipulumutso mwa ciyeretso ca Mzimu ndi cikhulupiriro ca coonadi;