1. PAULO, ndi Silvano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu:
2. Cisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Kristu.
3. Tiziyamika Mulungu nthawi zonse cifukwa ca inu, abale, monga kuyenera; pakuti cikhulupiriro canu cikula cikulire, ndipo cicurukira cikondanoca inu nonse, yense pa mnzace;