9. Pakuti mudziwa cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti, cifukwa ca inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwace mukakhale olemera.
10. Ndipo m'menemo odichula coyesa ine; pakuti cimene cipindulira inu, amene munayamba kale caka capitaci si kucita kokha, komanso kufunira.
11. Koma tsopano tsirizani kucitaku; kuti monga kunali cibvomerezo ca kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwacem'cimene muli naco.