23. Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wocita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Kristu.
24. Cifukwa cace muwatsimikizire iwo citsimikizo ca cikondi canu, ndi ca kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo.